Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 34:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Kenako mudzatenga ena mwa ana awo aakazi kuti akhale akazi a ana anu aamuna,+ ndipo ana awo aakazi adzachita chiwerewere ndi milungu yawo, n’kuchititsa ana anu aamuna kuchita chiwerewere ndi milungu yawo.+

  • Yoswa 23:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “Koma mukatembenuka+ n’kumamatira zotsala za anthu awa a mitundu ina,+ amene atsala pakati panuwa, kumakwatirana nawo,+ n’kumakhala pakati pawo, iwonso n’kumakhala pakati panu,

  • Ezara 9:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Choncho musakapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna,+ kapena kutenga ana awo aakazi n’kuwapereka kwa ana anu aamuna. Ndipo mpaka kalekale, musakawathandize kukhala ndi mtendere+ ndiponso kutukuka. Mukachite zimenezi kuti mukakhale amphamvu+ ndiponso kuti mukadyedi zabwino za dzikolo ndi kulitengadi kuti likhale la ana anu mpaka kalekale.’+

  • Ezara 10:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Kenako Sekaniya mwana wa Yehiela+ wochokera mwa ana a Elamu+ anauza Ezara kuti: “Ifeyo tachita zosakhulupirika kwa Mulungu wathu, chifukwa tinatenga akazi achilendo kuchokera kwa anthu a mitundu ina.+ Koma tsopano Aisiraeli ali ndi chiyembekezo+ pa nkhani imeneyi.

  • 2 Akorinto 6:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Musamangidwe m’goli ndi osakhulupirira, chifukwa ndinu osiyana.+ Pali ubale wotani pakati pa chilungamo ndi kusamvera malamulo?+ Kapena pali kugwirizana kotani pakati pa kuwala ndi mdima?+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena