16 Ukadzozenso Yehu+ mdzukulu wa Nimusi+ kuti akhale mfumu ya Isiraeli, ndipo Elisa+ mwana wa Safati wa ku Abele-mehola,+ ukam’dzoze kuti akhale mneneri m’malo mwa iwe.+
15 Ana a aneneri amene anali ku Yeriko atamuona chapatali, ananena kuti: “Tsopano mzimu+ wa Eliya uli pa Elisa.” Chotero anapita kukakumana naye n’kugwada+ pamaso pake mpaka nkhope zawo pansi.