Levitiko 26:30 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 30 Ndipo ndidzafafaniza malo anu opatulika olambirirako+ ndi kugwetsa maguwa anu ofukizirapo zonunkhira. Ndidzaponya mitembo yanu pamwamba pa mafano anu onyansa* opanda moyowo,+ ndipo mudzakhala onyansa kwa ine.+ Numeri 33:52 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 52 Mukapitikitse anthu onse a m’dzikolo, ndipo mukawononge zifaniziro zawo zonse zamiyala,+ ndi mafano awo onse achitsulo.+ Mukawonongenso malo awo onse opatulika olambirira.+ 1 Mafumu 3:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Anthuwo anali kupereka nsembe pamalo okwezeka,+ chifukwa anali asanamange nyumba ya dzina la Yehova mpaka masiku amenewo.+ 2 Mafumu 14:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Koma sanachotse malo okwezeka.+ Anthu anali kufukizabe ndi kupereka nsembe yautsi m’malo okwezekawo.+ Salimo 78:58 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 58 Iwo anapitiriza kumukhumudwitsa ndi malo awo okwezeka,+Ndipo anamuchititsa nsanje ndi zifaniziro zawo zogoba.+
30 Ndipo ndidzafafaniza malo anu opatulika olambirirako+ ndi kugwetsa maguwa anu ofukizirapo zonunkhira. Ndidzaponya mitembo yanu pamwamba pa mafano anu onyansa* opanda moyowo,+ ndipo mudzakhala onyansa kwa ine.+
52 Mukapitikitse anthu onse a m’dzikolo, ndipo mukawononge zifaniziro zawo zonse zamiyala,+ ndi mafano awo onse achitsulo.+ Mukawonongenso malo awo onse opatulika olambirira.+
2 Anthuwo anali kupereka nsembe pamalo okwezeka,+ chifukwa anali asanamange nyumba ya dzina la Yehova mpaka masiku amenewo.+
4 Koma sanachotse malo okwezeka.+ Anthu anali kufukizabe ndi kupereka nsembe yautsi m’malo okwezekawo.+
58 Iwo anapitiriza kumukhumudwitsa ndi malo awo okwezeka,+Ndipo anamuchititsa nsanje ndi zifaniziro zawo zogoba.+