4 koma osabwera nayo pakhomo la chihema chokumanako,+ kuti aipereke monga nsembe kwa Yehova patsogolo pa chihema cha Yehova, ameneyo adzakhala ndi mlandu wa magazi. Munthu ameneyo wakhetsa magazi, ndipo ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.+
30 Ndipo ndidzafafaniza malo anu opatulika olambirirako+ ndi kugwetsa maguwa anu ofukizirapo zonunkhira. Ndidzaponya mitembo yanu pamwamba pa mafano anu onyansa* opanda moyowo,+ ndipo mudzakhala onyansa kwa ine.+
6 Nsembe zanu zopsereza+ ndi nsembe zina, zopereka zanu za chakhumi,*+ chopereka chochokera m’manja mwanu,+ nsembe zanu za lonjezo,+ nsembe zanu zaufulu,+ ana oyamba kubadwa a ng’ombe ndi a nkhosa zanu,+ zonsezi muzidzazibweretsa kumalo amenewo.