Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 32:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Anayamba kuputa nsanje+ yake ndi milungu yachilendo.+

      Anapitiriza kumukhumudwitsa ndi zinthu zonyansa.+

  • Oweruza 2:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Iwo anasiya Yehova, Mulungu wa makolo awo amene anawatulutsa m’dziko la Iguputo,+ n’kuyamba kutsatira milungu ina mwa milungu ya anthu owazungulira.+ Anayamba kugwadira milungu imeneyo, moti anakhumudwitsa Yehova.+

  • 1 Samueli 7:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Zitatero, Samueli anauza nyumba yonse ya Isiraeli kuti: “Ngati mukubwereradi kwa Yehova+ ndi mtima wanu wonse, chotsani milungu yachilendo pakati panu.+ Muchotsenso zifaniziro za Asitoreti,+ ndi kulunjikitsa mitima yanu kwa Yehova mosayang’ananso kwina,+ ndi kutumikira iye yekha. Mukatero, adzakupulumutsani m’manja mwa Afilisiti.”+

  • 1 Mafumu 11:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Panali pa nthawi imeneyi pamene Solomo anamangira Kemosi+ malo okwezeka,+ chinthu chonyansa+ cha Mowabu, paphiri+ lomwe linali patsogolo+ pa Yerusalemu. Anamangiranso Moleki malo okwezeka, yemwe ndi chinthu chonyansa cha ana a Amoni.

  • 1 Mafumu 12:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Choncho mfumuyo inakambirana ndi anthu ena+ n’kupanga ana awiri a ng’ombe agolide.+ Itatero inauza anthuwo kuti: “N’zovuta kwambiri kwa inu kuti muzipita ku Yerusalemu. Nayu Mulungu wanu+ Aisiraeli inu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo.”+

  • 2 Mafumu 21:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Komanso iye anaika m’nyumbayo chifaniziro+ cha mzati wopatulika chimene anapanga. Koma ponena za nyumba imeneyo,+ Yehova anauza Davide ndi Solomo mwana wake kuti: “M’nyumba iyi ndiponso mu Yerusalemu mzinda umene ndausankha pa mafuko onse a Isiraeli, ndidzaikamo dzina langa mpaka kalekale.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena