32Pambuyo pa zimenezi ndiponso pambuyo pa ntchito zokhulupirika+ za Hezekiya, Senakeribu+ mfumu ya Asuri+ anabwera n’kudzazungulira Yuda ndipo anamanga misasa pafupi ndi mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ Iye anali kuganiza zogonjetsa mizindayo kuti ikhale yake.
36M’chaka cha 14 cha Mfumu Hezekiya, Senakeribu+ mfumu ya Asuri+ anabwera kudzachita nkhondo ndi mizinda yonse ya Ayuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, ndipo analanda mizindayo.+