18 Mulungu wanga, tcherani khutu lanu kuti mumve.+ Tsegulani maso anu kuti muone kuwonongeka kwathu ndi kwa mzinda wotchedwa ndi dzina lanu.+ Ifeyo tikukuchondererani, osati chifukwa cha zochita zathu zolungama,+ koma chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.+