13 ‘Nyumba za mu Yerusalemu ndi nyumba za mafumu a Yuda zidzakhala zodetsedwa ngati Tofeti.+ Zimenezi ndi nyumba zonse zimene pamadenga ake anali kufukizirapo nsembe zautsi kwa makamu akumwamba+ ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa milungu ina.’”+
5 Ndidzafafaniza anthu amene akugwadira khamu la zinthu zakuthambo pamadenga* a nyumba zawo,+ ndiponso amene akugwada ndi kulumbira+ kuti adzakhala okhulupirika kwa Yehova+ koma amakhalanso akulumbira m’dzina la Malikamu.+