12 Kenako mfumuyo inagumula maguwa ansembe amene anali padenga la chipinda chapadenga+ cha Ahazi, amene mafumu a Yuda anamanga. Inagumulanso maguwa ansembe+ amene Manase anamanga pamabwalo awiri a nyumba ya Yehova. Itatero, inawaperapera komweko ndipo fumbi lake inakaliwaza kuchigwa cha Kidironi.