3 M’chaka cha 8 cha ulamuliro wa Yosiya, iye akadali mnyamata,+ anayamba kufunafuna+ Mulungu wa Davide kholo lake. M’chaka cha 12 anayamba kuyeretsa+ Yuda ndi Yerusalemu pochotsa malo okwezeka,+ mizati yopatulika,+ zifaniziro zogoba,+ ndi zifaniziro zopangidwa ndi zitsulo zosungunula.