15 Kenako anauza anthuwo kuti: “Khalani maso ndipo chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwamtundu uliwonse,+ chifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.”+
10 Pakuti kukonda+ ndalama ndi muzu+ wa zopweteka za mtundu uliwonse,+ ndipo pokulitsa chikondi chimenechi, ena asocheretsedwa n’kusiya chikhulupiriro ndipo adzibweretsera zopweteka zambiri pathupi lawo.+