Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 6:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Pamenepo, Yehova anaona kuti kuipa kwa anthu kwachuluka padziko lapansi, ndipo malingaliro+ onse a m’mitima ya anthu anali oipa okhaokha nthawi zonse.+

  • Genesis 8:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Ndiyeno Yehova anamva fungo lokhazika mtima pansi,+ moti ananena mumtima+ mwake kuti: “Sindidzatembereranso nthaka+ chifukwa cha zochita za anthu, popeza maganizo+ a anthu amakhala oipa kuyambira pa ubwana wawo.+ Ndipo sindidzawononganso chilichonse monga ndachitiramu.+

  • Miyambo 28:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Munthu wodalira mtima wake ndi wopusa,+ koma woyenda mwanzeru ndi amene adzapulumuke.+

  • Yesaya 44:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Iye akudya phulusa.+ Mtima wake umene wanyengedwa wamusocheretsa.+ Iye sakupulumutsa moyo wake kapena kunena kuti: “Kodi chinthu chimene chili m’dzanja langa lamanjachi si chonyenga?”+

  • Yesaya 59:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Ife taphwanya malamulo ndipo tamukana Yehova.+ Tabwerera m’mbuyo n’kumusiya Mulungu wathu. Tanena zinthu zopondereza ena ndi zopanduka.+ Taganiza mawu achinyengo mumtima mwathu n’kumawalankhula chapansipansi.+

  • Yakobo 1:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Koma munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako chake.+

  • Yakobo 1:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Ngati munthu akudziona ngati wopembedza,+ koma salamulira lilime lake,+ ndipo akupitiriza kunyenga mtima wake,+ kupembedza kwa munthu ameneyu n’kopanda pake.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena