1 Samueli 8:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Atafika kumeneko anamuuza kuti: “Iweyo wakalamba, koma ana ako sakutsatira chitsanzo chako. Ndiye tikufuna kuti utiikire mfumu+ yoti izitiweruza ngati mitundu ina yonse.” 2 Samueli 14:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Pamenepo mkazi wa ku Tekowa uja anapita kukaonana ndi mfumu, ndipo anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi,+ kenako anadzigwetsa pansi, n’kunena kuti: “Chonde mfumu, ndipulumutseni!”+ 2 Mafumu 6:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Mfumu ya Isiraeli ikuyenda pamwamba pa khoma, mayi wina analankhula mokweza kwa mfumuyo kuti: “Ndithandizeni mbuyanga mfumu!”+ Luka 18:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Koma mumzindawo munali mkazi wina wamasiye ndipo anali kupitapita+ kwa woweruza uja kukamupempha kuti, ‘Ndiweruzireni mlandu wanga ndi munthu amene akutsutsana nane, kuti pachitike chilungamo.’
5 Atafika kumeneko anamuuza kuti: “Iweyo wakalamba, koma ana ako sakutsatira chitsanzo chako. Ndiye tikufuna kuti utiikire mfumu+ yoti izitiweruza ngati mitundu ina yonse.”
4 Pamenepo mkazi wa ku Tekowa uja anapita kukaonana ndi mfumu, ndipo anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi,+ kenako anadzigwetsa pansi, n’kunena kuti: “Chonde mfumu, ndipulumutseni!”+
26 Mfumu ya Isiraeli ikuyenda pamwamba pa khoma, mayi wina analankhula mokweza kwa mfumuyo kuti: “Ndithandizeni mbuyanga mfumu!”+
3 Koma mumzindawo munali mkazi wina wamasiye ndipo anali kupitapita+ kwa woweruza uja kukamupempha kuti, ‘Ndiweruzireni mlandu wanga ndi munthu amene akutsutsana nane, kuti pachitike chilungamo.’