17 Komanso, adzatsogola monga kalambulabwalo wa Mulungu ali ndi mzimu ndi mphamvu ngati za Eliya.+ Iye adzatembenuza mitima+ ya abambo kuti ikhale ngati ya ana, ndipo osamvera adzawatembenuzira ku nzeru yeniyeni ya anthu olungama. Adzachita izi kuti asonkhanitsire Yehova+ anthu okonzedwa.”+