23 M’chaka cha 15 cha Amaziya mwana wa Yehoasi mfumu ya Yuda, Yerobowamu+ mwana wa Yehoasi mfumu ya Isiraeli anakhala mfumu ku Samariya, ndipo analamulira zaka 41.
12 Izi zinakwaniritsa mawu a Yehova+ amene anawalankhula kwa Yehu, akuti:+ “Ana+ ako aamuna adzakhala pampando wachifumu wa Isiraeli mpaka m’badwo wachinayi.” Ndipo zinaterodi.+
10 Pakuti Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake,+ mwa kutumikira oyera+ ndipo mukupitiriza kuwatumikira.