1 Awa ndi mawu a Amosi amene anali mmodzi mwa anthu oweta nkhosa ku Tekowa.+ Anauzidwa mawu amenewa m’masomphenya okhudza Isiraeli,+ m’masiku a Uziya+ mfumu ya Yuda ndi m’masiku a Yerobowamu+ mwana wa Yowasi,+ mfumu ya Isiraeli, zaka ziwiri chivomezi chisanachitike.+