-
1 Samueli 16:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Patapita nthawi, Yehova anauza Samueli kuti: “Kodi ulirira Sauli+ mpaka liti, pamene ine ndamukana kuti alamulire monga mfumu ya Isiraeli?+ Thira mafuta m’nyanga yako+ ndipo unyamuke. Ndikutumiza kwa Jese+ wa ku Betelehemu, chifukwa ndapeza munthu pakati pa ana ake aamuna woti akhale mfumu yanga.”+
-
-
Mika 5:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 “Iwe Betelehemu Efurata,+ ndiwe mzinda waung’ono kwambiri moti sungawerengedwe ngati umodzi mwa mizinda ya fuko la Yuda.+ Komabe mwa iwe+ mudzatuluka munthu amene adzakhale wolamulira mu Isiraeli,+ amene adzachite chifuniro changa. Munthu ameneyu wakhala alipo kuyambira nthawi zoyambirira, wakhala alipo kuyambira masiku akalekale.+
-