3 Choncho akulu onse a Isiraeli anabwera kwa mfumu ku Heburoni, ndipo Davide anachita nawo pangano ku Heburoni pamaso pa Yehova. Kenako iwo anadzoza+ Davide kukhala mfumu ya Isiraeli, mogwirizana ndi mawu a Yehova+ amene analankhula kudzera mwa Samueli.+