12 “Ukamachita kalembera pa ana a Isiraeli, + aliyense wa iwo azipereka dipo la moyo wake kwa Yehova pa nthawi yowawerengayo,+ kuti mliri usawagwere pochita kalemberayo.+
13 Owerengedwa onse ayenera kupereka zotsatirazi: hafu ya sekeli yolingana ndi sekeli la kumalo oyera.*+ Magera* 20 amakwana sekeli limodzi. Hafu ya sekeli ndi chopereka kwa Yehova.+
16 Choncho ulandire ndalama zasiliva zophimbira machimo kwa ana a Isiraeli ndi kuzipereka kuti zikagwiritsidwe ntchito pa utumiki wa pachihema chokumanako+ monga dipo la miyoyo yanu, pophimba machimo anu, kuti Yehova akumbukire ana a Isiraeli.”