16 Pamenepo anthu anatuluka ndi kukatenga zinthu zimenezi ndipo anapangira misasa. Aliyense anapanga msasa pamwamba pa nyumba yake+ komanso m’mabwalo awo, m’mabwalo+ a nyumba ya Mulungu woona, m’bwalo lalikulu+ la Chipata cha Kumadzi+ ndiponso m’bwalo lalikulu la Chipata cha Efuraimu.+
39 Anadutsanso pamwamba pa Chipata cha Efuraimu,+ Chipata cha Mzinda Wakale,+ Chipata cha Nsomba+ mpaka kukafika pa Nsanja ya Hananeli,+ Nsanja ya Meya+ ndi ku Chipata cha Nkhosa,+ ndipo anaima pa Chipata cha Alonda.