13 Mfumu ya Babulo inatenga chuma chonse cha m’nyumba ya Yehova ndi chuma cha m’nyumba ya mfumu.+ Inaphwanyaphwanyanso ziwiya zonse+ zagolide zimene Solomo mfumu ya Isiraeli anapangira kachisi wa Yehova, monga momwe Yehova ananenera.
7 Komanso, Mfumu Koresi inabweretsa ziwiya za nyumba ya Yehova.+ Ziwiyazo n’zimene Nebukadinezara anatenga ku Yerusalemu+ n’kukaziika m’kachisi wa mulungu wake.+
3 Pa zaka ziwiri zokha ndibwezeretsa pamalo ano ziwiya zonse za m’nyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara mfumu ya Babulo+ anatenga pamalo ano ndi kupita nazo ku Babulo.’”