13 Hezekiya anawamvetsera anthuwo ndipo anawaonetsa zonse za m’nyumba yake yosungiramo chuma.+ Anawaonetsa siliva, golide,+ mafuta a basamu,+ mafuta abwino, nyumba yake yosungiramo zida zankhondo, ndi chuma chake chonse. Palibe chimene Hezekiya sanawaonetse m’nyumba yake ndi mu ufumu wake wonse.+