13 Mfumu ya Babulo inatenga chuma chonse cha m’nyumba ya Yehova ndi chuma cha m’nyumba ya mfumu.+ Inaphwanyaphwanyanso ziwiya zonse+ zagolide zimene Solomo mfumu ya Isiraeli anapangira kachisi wa Yehova, monga momwe Yehova ananenera.
13 Zipilala+ zamkuwa zimene zinali m’nyumba ya Yehova, zotengera zokhala ndi mawilo+ ndi chosungiramo madzi chamkuwa+ zimene zinali m’nyumba ya Yehova, Akasidi anaziphwanyaphwanya n’kutenga mkuwa wake kupita nawo ku Babulo.+
18 Mfumuyo inatenga ziwiya zonse,+ zazikulu+ ndi zazing’ono, za m’nyumba ya Mulungu woona. Inatenganso chuma+ cha m’nyumba ya Yehova, chuma cha mfumu+ ndi cha akalonga ake. Inatenga chilichonse n’kupita nacho ku Babulo.
21 Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena mawu okhudza ziwiya zimene zinatsala m’nyumba ya Yehova, m’nyumba ya mfumu ya Yuda ndi zimene zinatsala ku Yerusalemu+ kuti,
2 Kenako Yehova anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda m’manja mwake.+ Anaperekanso kwa iye zina mwa ziwiya+ za m’nyumba ya Mulungu woona moti Nebukadinezara anazitengera kudziko la Sinara,+ kunyumba ya mulungu wake. Ziwiya zimenezi anakaziika m’nyumba ya mulungu wake yosungiramo chuma.+