3 Ndiyeno anauza Alevi, alangizi+ a Isiraeli yense, omwe anali oyera kwa Yehova, kuti: “Ikani Likasa lopatulika+ m’nyumba+ imene Solomo mwana wa Davide mfumu ya Isiraeli anamanga. Lisakhalenso katundu wolemera pamapewa anu.+ Tsopano tumikirani+ Yehova Mulungu wanu ndi anthu ake Aisiraeli.