10 Ndiyeno Aroni atangomaliza kulankhula ndi khamu lonse la ana a Isiraeli, iwo anatembenuka ndi kuyang’ana kuchipululu. Ndipo taonani! Ulemerero wa Yehova unaonekera mumtambo.+
4 Tsopano ulemerero wa Yehova+ unachoka pa akerubi n’kupita pakhomo la nyumba yopatulika, ndipo mtambo+ unadzaza nyumbayo pang’onopang’ono. Komanso ulemerero wowala wa Yehova unadzaza m’bwalo lonse la nyumbayo.