16 Ndiyeno ndinalankhula ndi ansembe ndi anthu ena onsewa kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Musamvere mawu a aneneri anu amene akulosera kwa inu kuti: “Taonani! Ziwiya za m’nyumba ya Yehova zibwezedwa kuchokera ku Babulo posachedwapa!”+ Pakuti iwo akulosera kwa inu monama.+