9 “‘Ndinawononga mbewu zanu ndi mphepo yotentha komanso ndi matenda a chuku.+ Munachulukitsa minda yanu ya mpesa ndi ya mbewu zina ndipo mbozi zinawononga mitengo yanu ya mkuyu ndi ya maolivi,+ komabe inu simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.
17 Anthu inu, ine ndinawononga mbewu zanu ndi mphepo yotentha,+ matenda a chuku+ ndi matalala.+ Zimenezi zinawononganso ntchito zonse za manja anu.+ Koma panalibe aliyense wa inu amene anabwerera kwa ine,’+ watero Yehova.