8 Choncho Hiramu anatumiza uthenga kwa Solomo, kuti: “Ndamva uthenga wanu. Ineyo ndichita zonse zimene mukufuna pa nkhani ya mitengo ya mkungudza ndiponso mitengo ina yofanana ndi mkungudza.+
5 Nyumba yaikuluyo anaikuta+ ndi matabwa a mitengo yofanana ndi mkungudza, kenako anaikutanso ndi golide wabwino.+ Atatero, anaikongoletsa ndi zithunzi za mitengo yakanjedza+ zojambula mochita kugoba ndiponso matcheni.+