8 Ku Yerusalemu nakonso Yehosafati anaikako Alevi ena,+ ansembe,+ ndi ena mwa atsogoleri a nyumba za makolo+ a Isiraeli, kuti azionetsetsa kuti anthu akutsatira chilamulo+ cha Yehova ndi kuti aziweruza milandu+ ya anthu a ku Yerusalemu.
20M’chaka cha 7, m’mwezi wachisanu, pa tsiku la 10 la mweziwo, akuluakulu a Isiraeli anabwera kwa ine kudzafunsira kwa Yehova,+ ndipo anakhala pamaso panga.+