6 Ezara ameneyu ananyamuka n’kuchoka ku Babulo. Iye anali katswiri wodziwa kukopera+ chilamulo cha Mose,+ chimene Yehova Mulungu wa Isiraeli anapereka. Chotero mfumu inamupatsa zopempha zake zonse chifukwa dzanja la Yehova Mulungu wake linali pa iye.+
2 Choncho Ezara wansembe+ anabweretsa chilamulo pamaso pa mpingo+ wa amuna komanso akazi ndi ana onse amene akanatha kumvetsera ndi kuzindikira+ zimene zinali kunenedwa. Limeneli linali tsiku loyamba la mwezi wa 7.+