3 Koma Zerubabele, Yesuwa,+ ndi atsogoleri ena onse+ a nyumba za makolo za Isiraeli anawayankha kuti: “Mulibe ufulu womanga nafe limodzi nyumba ya Mulungu wathu,+ pakuti ifeyo patokha timangira limodzi nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli, monga momwe Mfumu Koresi+ ya Perisiya yatilamulira.”