-
2 Mbiri 36:23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 “Koresi mfumu ya Perisiya+ wanena kuti, ‘Yehova Mulungu wakumwamba wandipatsa+ maufumu onse a padziko lapansi. Iye wandituma kuti ndim’mangire nyumba ku Yerusalemu m’dziko la Yuda.+ Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira,+ Yehova Mulungu wake akhale naye.+ Choncho apite.’”+
-
-
Ezara 6:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 “M’chaka choyamba cha Mfumu Koresi,+ mfumuyo inaika lamulo lokhudza nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu lakuti: Ayuda amangenso nyumbayo kuti azikapereka nsembe+ kumeneko, ndipo amange maziko olimba. Nyumbayo kutalika kwake kuchokera pansi kufika pamwamba ikhale mikono* 60, ndiponso m’lifupi mwake ikhale mikono 60.+
-