Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 25:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “‘Ndiyeno zaka 70 zimenezo zikadzakwanira,+ ndidzabwezera mfumu ya Babulo ndi mtundu umenewo zolakwa zawo.+ Ndidzabwezera zolakwa za dziko la Akasidi+ ndipo dziko lawolo lidzakhala mabwinja mpaka kalekale,’+ watero Yehova.

  • Yeremiya 29:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ndidzakulolani kuti mundipeze,’+ watero Yehova. ‘Ndidzasonkhanitsa anthu a mtundu wanu amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kumayiko ena ndipo ndidzakusonkhanitsani kuchokera m’mitundu yonse ndi kumalo onse kumene ndakubalalitsirani,’+ watero Yehova. ‘Kenako ndidzakubwezeretsani kumalo amene ndinakuchotsani ndi kukupititsani ku ukapolo.’+

  • Yeremiya 33:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 M’malo amenewa mudzamveka mawu achikondwerero ndi achisangalalo.+ Mudzamveka mawu a mkwati ndi mawu a mkwatibwi, ndi mawu a anthu onena kuti: “Tamandani Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndi wabwino.+ Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale!”’+

      “‘Anthuwo azidzabweretsa nsembe yoyamikira kunyumba ya Yehova,+ pakuti ndidzabwezeretsa anthu a m’dzikoli amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina kuti akhalenso ngati mmene analili poyamba,’+ watero Yehova.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena