-
Levitiko 7:12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Ngati akupereka nsembeyo posonyeza kuyamikira,+ pamenepo azipereka nsembe yoyamikira pamodzi ndi mkate wozungulira woboola pakati, wopanda chofufumitsa, wothira mafuta. Aziperekanso timitanda ta mkate topyapyala topanda chofufumitsa, topaka mafuta,+ ndi mkate wozungulira woboola pakati, wothira mafuta, wophika ndi ufa wosalala wosakaniza bwino kwambiri ndi mafuta.
-
-
2 Mbiri 29:31Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
31 Pomalizira pake Hezekiya anati: “Tsopano mwayeneretsedwa kuti mukhale ansembe+ otumikira Yehova. Bweretsani nsembe zoyamikira+ ndi nsembe zina+ kunyumba ya Yehova.” Ndiyeno mpingowo unayamba kubweretsa nsembe zoyamikira ndi nsembe zina, ndipo aliyense wa mtima wofunitsitsa anali kubweretsa nsembe zopsereza.+
-