Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mbiri 36:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 “Koresi mfumu ya Perisiya+ wanena kuti, ‘Yehova Mulungu wakumwamba wandipatsa+ maufumu onse a padziko lapansi. Iye wandituma kuti ndim’mangire nyumba ku Yerusalemu m’dziko la Yuda.+ Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira,+ Yehova Mulungu wake akhale naye.+ Choncho apite.’”+

  • Ezara 1:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Koresi mfumu ya Perisiya wanena kuti,+ ‘Yehova Mulungu wakumwamba+ wandipatsa+ maufumu onse a padziko lapansi. Iye wandituma kuti ndim’mangire nyumba ku Yerusalemu+ m’dziko la Yuda.

  • Ezara 6:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 “M’chaka choyamba cha Mfumu Koresi,+ mfumuyo inaika lamulo lokhudza nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu lakuti: Ayuda amangenso nyumbayo kuti azikapereka nsembe+ kumeneko, ndipo amange maziko olimba. Nyumbayo kutalika kwake kuchokera pansi kufika pamwamba ikhale mikono* 60, ndiponso m’lifupi mwake ikhale mikono 60.+

  • Yesaya 45:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 “Ine ndautsa winawake m’chilungamo+ ndipo njira zake zonse ndidzaziwongola.+ Iye ndi amene adzamange mzinda wanga+ ndipo anthu anga amene ali ku ukapolo adzawamasula,+ koma osati ndi malipiro+ kapena ndi chiphuphu,” watero Yehova wa makamu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena