Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 75:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Mulungu ndiye woweruza.+

      Amatsitsa wina ndi kukweza wina.+

  • Yeremiya 27:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 ‘Ine ndinapanga dziko lapansi,+ anthu+ ndi nyama+ zapadziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu zanga zazikulu+ ndiponso dzanja langa lotambasula.+ Ndipo dzikoli ndalipereka kwa amene ndikufuna.+

  • Danieli 2:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Iye amasintha nthawi ndi nyengo,+ amachotsa mafumu ndi kuika mafumu,+ amapereka nzeru kwa anthu anzeru ndiponso amachititsa kuti anthu ozindikira adziwe zinthu.+

  • Danieli 4:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Iye amaona anthu onse okhala padziko lapansi ngati opanda pake+ ndipo amachita zinthu mogwirizana ndi chifuniro chake pakati pa makamu akumwamba ndi pakati pa anthu okhala padziko lapansi.+ Palibe aliyense amene angaletse dzanja+ lake kapena kumufunsa kuti, ‘Mukuchita chiyani?’+

  • Danieli 5:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Iye anathamangitsidwa pakati pa anthu ndipo mtima wake unasinthidwa n’kukhala ngati wa nyama. Anayamba kukhala limodzi ndi abulu akutchire+ ndipo anali kudya udzu ngati ng’ombe. Thupi lake linkanyowa ndi mame akumwamba,+ kufikira pamene anadziwa kuti Wam’mwambamwamba ndiye Wolamulira wa maufumu a anthu, ndiponso kuti akafuna kuika munthu aliyense kuti akhale wolamulira, amamuika.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena