-
Esitere 2:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Ndiyeno inu mfumu musankhe anthu m’zigawo zonse+ za ufumu wanu. Anthuwo asonkhanitse pamodzi atsikana onse, anamwali okongola, kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani,+ m’nyumba ya akazi imene Hegai+ akuyang’anira. Iye ndi munthu wofulidwa wa mfumu+ woyang’anira akazi, amenenso ndi mkulu woyang’anira nyumba ya akazi. Ndipo kumeneko atsikanawo azikawapaka mafuta okongoletsa.
-
-
Esitere 2:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Madzulo mtsikanayo anali kubwera kwa mfumu, ndipo m’mawa anali kubwerera kunyumba yachiwiri ya akazi, imene Sasigazi anali kuyang’anira. Sasigazi anali munthu wofulidwa wa mfumu,+ mkulu woyang’anira akazi. Mtsikanayo sanalinso kubwera kwa mfumu pokhapokha ngati mfumuyo yakondwera naye ndipo yamuitanitsa mwa kum’tchula dzina.+
-