1 Samueli 12:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Chifukwa cha dzina lake lalikulu,+ Yehova sadzasiya+ anthu ake, pakuti Yehova wafuna kuti inuyo mukhale anthu ake.+ Yesaya 54:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana,+ ndipo lilime lililonse limene lidzalimbane nawe pamlandu udzalitsutsa.+ Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova,+ ndipo chilungamo chawo n’chochokera kwa ine,” akutero Yehova.+ Yeremiya 30:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 “Pakuti ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse,”+ watero Yehova. “Ndidzawononga anthu a mitundu yonse ya kumene ndinakubalalitsirani,+ koma iwe sindidzakuwononga.+ Ndidzakuwongolera pa mlingo woyenera chifukwa sindidzakusiya osakulanga.”+ Amosi 9:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 “Yehova wanena kuti, ‘Taonani, ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndikuyang’ana ufumu wochimwawo,+ ndipo ndidzaufafaniza panthaka ya dziko lapansi.+ Komabe nyumba ya Yakobo+ sindidzaifafaniza yonse.
22 Chifukwa cha dzina lake lalikulu,+ Yehova sadzasiya+ anthu ake, pakuti Yehova wafuna kuti inuyo mukhale anthu ake.+
17 Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana,+ ndipo lilime lililonse limene lidzalimbane nawe pamlandu udzalitsutsa.+ Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova,+ ndipo chilungamo chawo n’chochokera kwa ine,” akutero Yehova.+
11 “Pakuti ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse,”+ watero Yehova. “Ndidzawononga anthu a mitundu yonse ya kumene ndinakubalalitsirani,+ koma iwe sindidzakuwononga.+ Ndidzakuwongolera pa mlingo woyenera chifukwa sindidzakusiya osakulanga.”+
8 “Yehova wanena kuti, ‘Taonani, ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndikuyang’ana ufumu wochimwawo,+ ndipo ndidzaufafaniza panthaka ya dziko lapansi.+ Komabe nyumba ya Yakobo+ sindidzaifafaniza yonse.