-
Esitere 5:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Pamenepo mkazi wake Zeresi ndi anzake onsewo anamuuza kuti: “Mukonzetse mtengo+ wotalika mikono* 50. Ndiyeno m’mawa+ mukauze mfumu kuti apachike Moredekai pamtengowo.+ Mukatero mupite kuphwando ndi mfumu muli wosangalala.” Zimenezi zinaoneka zosangalatsa+ kwa Hamani, choncho anakonzetsa mtengowo.+
-
-
Esitere 7:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Haribona,+ mmodzi mwa nduna za panyumba ya mfumu+ amene anali pamaso pa mfumu anati: “Palinso mtengo+ umene Hamani anapangira Moredekai, amene analankhula zabwino za mfumu.+ Mtengowu uli m’nyumba ya Hamani ndipo ndi wotalika mikono 50.” Pamenepo mfumu inati: “Amuna inu, kam’pachikeni pamtengo umenewo.”+
-