Salimo 7:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Nyamukani, inu Yehova, mu mkwiyo wanu.+Imirirani ndi kukhaulitsa amene andisonyeza mkwiyo ndi kundichitira zoipa.+Dzukani ndi kundithandiza,+ pakuti mwalamula kuti chiweruzo chiperekedwe.+ Salimo 9:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Anthu a mitundu ina agwera m’dzenje limene anakumba okha.+Phazi lawo lakodwa mu ukonde+ umene anatchera okha.+ Salimo 35:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Awonongeke pamene iwo sakuyembekezera,+Akodwe mu ukonde umene atchera okha.+Agweremo ndi kuwonongeka.+ Salimo 73:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Haa! M’kanthawi kochepa, iwo akhala chinthu chodabwitsa.+Afika pamapeto awo ndipo atha chifukwa cha masoka owagwera modzidzimutsa! Miyambo 11:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Kulungama kwa anthu owongoka mtima n’kumene kudzawapulumutse,+ koma anthu ochita zinthu mwachinyengo adzagwidwa ndi zolakalaka zawo.+
6 Nyamukani, inu Yehova, mu mkwiyo wanu.+Imirirani ndi kukhaulitsa amene andisonyeza mkwiyo ndi kundichitira zoipa.+Dzukani ndi kundithandiza,+ pakuti mwalamula kuti chiweruzo chiperekedwe.+
15 Anthu a mitundu ina agwera m’dzenje limene anakumba okha.+Phazi lawo lakodwa mu ukonde+ umene anatchera okha.+
8 Awonongeke pamene iwo sakuyembekezera,+Akodwe mu ukonde umene atchera okha.+Agweremo ndi kuwonongeka.+
19 Haa! M’kanthawi kochepa, iwo akhala chinthu chodabwitsa.+Afika pamapeto awo ndipo atha chifukwa cha masoka owagwera modzidzimutsa!
6 Kulungama kwa anthu owongoka mtima n’kumene kudzawapulumutse,+ koma anthu ochita zinthu mwachinyengo adzagwidwa ndi zolakalaka zawo.+