Miyambo 3:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Usamadzione kuti ndiwe wanzeru.+ Uziopa Yehova ndi kupatuka pa choipa.+ Mateyu 11:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Pa nthawi imeneyo Yesu ananena kuti: “Ndikutamanda inu Atate pamaso pa onse, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa mwabisira zinthu zimenezi anthu anzeru ndi ozindikira ndipo mwaziulula kwa tiana.+ Aroma 11:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 N’zoonadi! Iwo anadulidwa chifukwa chakuti analibe chikhulupiriro,+ koma iweyo waimirira chifukwa cha chikhulupiriro.+ Taya maganizo odzikuzawo,+ koma khala ndi mantha.+ Aroma 12:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Muziona ena mmene inuyo mumadzionera.+ Musamaganize modzikweza,+ koma khalani ndi mtima wodzichepetsa.+ Musadziyese anzeru.+ 1 Akorinto 1:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Mukuona mmene anakuitanirani, abale, kuti si ambiri amene anthu amawaona kuti ndi anzeru+ omwe anaitanidwa,+ si ambiri amphamvu+ amene anaitanidwa, si ambiri a m’mabanja achifumu.
25 Pa nthawi imeneyo Yesu ananena kuti: “Ndikutamanda inu Atate pamaso pa onse, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa mwabisira zinthu zimenezi anthu anzeru ndi ozindikira ndipo mwaziulula kwa tiana.+
20 N’zoonadi! Iwo anadulidwa chifukwa chakuti analibe chikhulupiriro,+ koma iweyo waimirira chifukwa cha chikhulupiriro.+ Taya maganizo odzikuzawo,+ koma khala ndi mantha.+
16 Muziona ena mmene inuyo mumadzionera.+ Musamaganize modzikweza,+ koma khalani ndi mtima wodzichepetsa.+ Musadziyese anzeru.+
26 Mukuona mmene anakuitanirani, abale, kuti si ambiri amene anthu amawaona kuti ndi anzeru+ omwe anaitanidwa,+ si ambiri amphamvu+ amene anaitanidwa, si ambiri a m’mabanja achifumu.