Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yobu 27:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ngakhale akonze zovalazo, wolungama ndi amene adzazivale.+

      Ndipo silivayo, wosalakwa ndi amene adzam’tenge.

  • Salimo 49:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pakuti amaona kuti ngakhale anthu anzeru amafa,+

      Wopusa ndi wopanda nzeru, onsewo amawonongeka,+

      Ndipo chuma chawo amasiyira anthu ena.+

  • Miyambo 13:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Munthu wabwino adzasiyira cholowa zidzukulu zake, ndipo chuma cha wochimwa chimasungidwa kuti chidzakhale cha munthu wolungama.+

  • Mlaliki 2:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Ndipo kodi ndani angadziwe kuti kaya adzakhala wanzeru kapena wopusa?+ Koma adzatenga zinthu zanga zonse zimene ndinazipeza movutikira ndiponso zimene ndinazichita mwanzeru padziko lapansi pano.+ Zimenezinso n’zachabechabe.

  • Mlaliki 4:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Pali munthu amene ali yekhayekha, wopanda mnzake.+ Alibenso mwana kapena m’bale wake,+ koma amangokhalira kugwira ntchito mwakhama. Komanso maso ake sakhutira ndi chuma.+ Iye amafunsa kuti: “Kodi ntchito yovutayi ndikugwirira ndani n’kumadzimana zinthu zabwino?”+ Izinso n’zachabechabe ndiponso ndi ntchito yosautsa mtima.+

  • Luka 12:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Koma Mulungu anamuuza kuti, ‘Wopanda nzeru iwe, usiku womwe uno moyo wako adzaufuna.+ Nanga chuma chimene waunjikachi chidzakhala cha ndani?’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena