Salimo 39:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Zoonadi, munthu amayenda ngati chithunzithunzi.+Ndithudi, anthu amapokosera pachabe.+Munthu amaunjika zinthu ndipo sadziwa amene adzazitute.+ Miyambo 11:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Zinthu zamtengo wapatali zidzakhala zopanda phindu pa tsiku la mkwiyo woopsa,+ koma chilungamo n’chimene chidzapulumutse munthu ku imfa.+ Miyambo 23:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Usamadzitopetse ndi ntchito kuti upeze chuma.+ Leka kudzidalira kuti ndiwe womvetsa zinthu.+ Mlaliki 2:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Ineyo ndinadana ndi ntchito yonse yovuta imene ndinali kugwira padziko lapansi pano,+ imene ndidzasiyire munthu amene akubwera pambuyo panga.+ Yeremiya 17:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Munthu wopeza chuma mopanda chilungamo+ ali ngati nkhwali imene yasonkhanitsa mazira amene sinaikire. Chuma chakecho adzachisiya asanakwanitse ngakhale hafu ya zaka za moyo wake,+ ndipo pamapeto pake adzaonekera kuti ndi wopusa.”+ Luka 12:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Koma Mulungu anamuuza kuti, ‘Wopanda nzeru iwe, usiku womwe uno moyo wako adzaufuna.+ Nanga chuma chimene waunjikachi chidzakhala cha ndani?’+
6 Zoonadi, munthu amayenda ngati chithunzithunzi.+Ndithudi, anthu amapokosera pachabe.+Munthu amaunjika zinthu ndipo sadziwa amene adzazitute.+
4 Zinthu zamtengo wapatali zidzakhala zopanda phindu pa tsiku la mkwiyo woopsa,+ koma chilungamo n’chimene chidzapulumutse munthu ku imfa.+
18 Ineyo ndinadana ndi ntchito yonse yovuta imene ndinali kugwira padziko lapansi pano,+ imene ndidzasiyire munthu amene akubwera pambuyo panga.+
11 Munthu wopeza chuma mopanda chilungamo+ ali ngati nkhwali imene yasonkhanitsa mazira amene sinaikire. Chuma chakecho adzachisiya asanakwanitse ngakhale hafu ya zaka za moyo wake,+ ndipo pamapeto pake adzaonekera kuti ndi wopusa.”+
20 Koma Mulungu anamuuza kuti, ‘Wopanda nzeru iwe, usiku womwe uno moyo wako adzaufuna.+ Nanga chuma chimene waunjikachi chidzakhala cha ndani?’+