Miyambo 28:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Munthu wochita zinthu mokhulupirika adzapeza madalitso ambiri,+ koma woyesetsa kuti apeze chuma mofulumira, sadzapitiriza kukhala wosalakwa.+ Yohane 6:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Musamagwire ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimawonongeka,+ koma kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chopereka moyo wosatha,+ chimene Mwana wa munthu adzakupatsani. Pakuti Atate, Mulungu yekhayo, waika chisindikizo pa iye chomuvomereza.”+ 1 Timoteyo 6:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Pakuti kukonda+ ndalama ndi muzu+ wa zopweteka za mtundu uliwonse,+ ndipo pokulitsa chikondi chimenechi, ena asocheretsedwa n’kusiya chikhulupiriro ndipo adzibweretsera zopweteka zambiri pathupi lawo.+
20 Munthu wochita zinthu mokhulupirika adzapeza madalitso ambiri,+ koma woyesetsa kuti apeze chuma mofulumira, sadzapitiriza kukhala wosalakwa.+
27 Musamagwire ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimawonongeka,+ koma kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chopereka moyo wosatha,+ chimene Mwana wa munthu adzakupatsani. Pakuti Atate, Mulungu yekhayo, waika chisindikizo pa iye chomuvomereza.”+
10 Pakuti kukonda+ ndalama ndi muzu+ wa zopweteka za mtundu uliwonse,+ ndipo pokulitsa chikondi chimenechi, ena asocheretsedwa n’kusiya chikhulupiriro ndipo adzibweretsera zopweteka zambiri pathupi lawo.+