Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Miyambo 10:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Chuma cha anthu oipa chidzakhala chopanda phindu,+ koma chilungamo n’chimene chidzapulumutse munthu ku imfa.+

  • Miyambo 18:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Zinthu zamtengo wapatali za munthu wachuma ndizo mzinda wake wolimba,+ ndipo m’maganizo mwake zili ngati mpanda woteteza.+

  • Ezekieli 7:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 “‘Siliva wawo adzamuponyera mumsewu ndipo golide wawo adzaipidwa naye. Siliva wawo kapena golide wawo sadzatha kuwapulumutsa m’tsiku la mkwiyo waukulu wa Yehova.+ Iwo sadzakhuta ndipo m’matumbo mwawo simudzadzaza, pakuti chumacho chakhala chowapunthwitsa ndiponso chowachititsa zolakwa.+

  • Zefaniya 1:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Siliva kapena golide wawo sadzawapulumutsa pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.+ Moto wa mkwiyo wake udzanyeketsa dziko lonse lapansi,+ chifukwa iye adzafafaniza anthu onse okhala padziko lapansi.”+

  • Mateyu 16:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Kodi munthu angapindulenji ngati atapeza zinthu zonse za m’dzikoli koma n’kutaya moyo wake?+ Kapena munthu angapereke chiyani chosinthanitsa+ ndi moyo wake?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena