Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ezekieli 13:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Dzanja langa lalimbana ndi aneneri amene akuona masomphenya abodza ndiponso amene akulosera zonama.+ Iwo sadzapitiriza kukhala m’gulu la anthu anga apamtima,+ komanso sadzalembedwa m’buku la mayina a anthu a nyumba ya Isiraeli.+ Sadzabwera kudziko la Isiraeli+ ndipo anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa,+

  • Afilipi 4:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ndikupempha iwenso wantchito mnzanga weniweni,+ kuti upitirize kuwathandiza amayi amenewa. Iwo ayesetsa limodzi ndi ine pa ntchito+ ya uthenga wabwino. Achita zimenezi limodzinso ndi Kilementi ndi antchito anzanga ena onse,+ amene mayina awo+ ali m’buku la moyo.+

  • Chivumbulutso 3:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Choncho amene wapambana pa nkhondo+ adzavekedwa malaya akunja oyera.+ Ndipo sindidzafafaniza dzina lake m’buku la moyo,+ koma ndidzavomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga,+ ndi pamaso pa angelo ake.+

  • Chivumbulutso 13:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Ndipo onse okhala padziko lapansi adzachilambira. Anthu onsewa mayina awo sanalembedwe mumpukutu+ wa moyo, umene Mwanawankhosa amene anaphedwa,+ ndiye mwiniwake. Mpukutuwo unakonzedwa kuchokera pa kukhazikitsidwa kwa dziko.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena