-
Yesaya 49:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Yehova, Wowombola Isiraeli,+ Woyera wake, wauza yemwe ananyozedwa kwambiri,+ yemwe amadedwa ndi mtundu wa anthu,+ mtumiki wa atsogoleri,+ kuti: “Mafumu adzaimirira chifukwa cha zimene adzaone,+ ndipo akalonga adzagwada chifukwa cha Yehova. Iye ndi wokhulupirika,+ Woyera wa Isiraeli, amene anakusankha.”+
-
-
Yesaya 60:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Pakuti zilumba zidzayembekezera ine.+ Nazonso zombo za ku Tarisi+ zidzayembekezera ine ngati poyamba paja, kuti zikubweretsere ana ako aamuna kuchokera kutali.+ Iwo adzabwera atanyamula siliva ndi golide wawo,+ kuti alemekeze dzina+ la Yehova Mulungu wako ndi Woyera wa Isiraeli,+ pakuti iye adzakhala atakukongoletsa.+
-