52Dzuka! Dzuka! Vala mphamvu zako+ iwe Ziyoni. Vala zovala zako zokongola+ iwe Yerusalemu, mzinda woyera.+ Pakuti mwa iwe simudzabweranso munthu wosadulidwa ndi wodetsedwa.+
5 Iwe udzaitana mtundu umene sukuudziwa,+ ndipo anthu a mtundu wosakudziwa adzathamangira kwa iwe+ chifukwa cha Yehova Mulungu wako,+ ndiponso chifukwa cha Woyera wa Isiraeli,+ pakuti iye adzakukongoletsa.+