Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 18:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Tsopano ndadziwa kuti Yehova ndiye wamkulu kuposa milungu ina yonse.+ Zimenezi zinaoneka Aiguputo atasonyeza kudzikuza pamaso pa Aisiraeli.”

  • Salimo 97:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Pakuti inu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba wolamulira dziko lonse lapansi.+

      Mwakwera pamwamba kwambiri kuposa milungu ina yonse.+

  • Salimo 135:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Ine ndikudziwa bwino kuti Yehova ndi wamkulu,+

      Ndipo Ambuye wathu ndi woposa milungu ina yonse.+

  • Yesaya 44:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Anthu inu musachite mantha ndipo musathedwe nzeru.+ Kodi sindinachititse aliyense wa inu kuti amve kuyambira nthawi imeneyo? Kodi sindinakuuzeni zimenezi?+ Inu ndinu mboni zanga.+ Kodi palinso Mulungu kupatulapo ine?+ Ayi, palibe Thanthwe.+ Sindikudziwapo aliyense.’”

  • Malaki 1:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 “Aliyense wochita zachinyengo popereka nsembe nyama yachilema ndi wotembereredwa. Iye amalonjeza ndi kupereka nsembe nyama yachilema kwa Yehova pamene nyama yamphongo yabwinobwino, ali nayo pagulu la ziweto zake.+ Ine ndine Mfumu yaikulu+ ndipo dzina langa lidzaopedwa pakati pa anthu a mitundu ina,”+ watero Yehova wa makamu.

  • 1 Akorinto 8:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 kwa ife Mulungu alipo mmodzi yekha basi+ amene ndi Atate.+ Iye ndi amene zinthu zonse zinachokera mwa iye, ndipo ifeyo ndife ake.+ Ndipo pali Ambuye+ mmodzi, Yesu Khristu,+ amene zinthu zonse zinakhalapo kudzera mwa iye,+ ndipo ifeyo kudzera mwa iyeyo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena