12 Ine ndidzadutsa m’dziko la Iguputo usiku umenewo+ ndi kupha mwana aliyense woyamba kubadwa m’dziko la Iguputo, mwana wa munthu kapena wa chiweto.+ Ndipo ndidzapereka ziweruzo pa milungu yonse ya mu Iguputo.+ Ine ndine Yehova.+
6 Koma ponena za nthawi imene adzatumize kachiwiri Mwana wake Woyamba kubadwayo+ padziko lapansi kumene kuli anthu, iye akuti: “Angelo+ onse a Mulungu amugwadire.”+